sábado, 30 de março de 2013

Mtsutso pa za makanda odabwitsa

Mtsutso pa za makanda odabwitsa
Muula: Moyo ndi chimodzimodzi
Mtsutso wakula ngati n’koyenera kuti ana obadwa modabwitsa azituluka m’chikuta.

Izi zadza mwana wina wankhope yodabwitsa atabadwa kuchipatala cha Salima sabata yatha. Mwanayo adamwalira Loweruka pachipatala cha Lilongwe. Izi zidachitika patangotha sabata zochepa kuchokera pomwe mwana winanso yemwe adabadwa wopanda maso, mphuno ndi makutu adabwadwa ku Nkhotakota. Uyonso adatisiya.
Pomwe ena akuti ndi bwino kutsatira zomwe zinkachitika kale, kuti ana otere samatuluka m’chikuta, ena akuti kutero n’kulakwa chifukwa ndi kuwaphera ufulu wokhala moyo anawo.
Mayi wina wa ku Chilomoni, mumzinda wa Blantyre, Martha Banda, akuti ngakhale akudziwa kuti kupha n’kulakwa, si bwino kulola anawo atuluke m’chikuta chifukwa adzazunzika.
Mzamba wina wodziwa zitsamba ku Mchinji, Ethel Kwitanda, wati kale ana otere sankatuluka m’chikuta koma pankachitika nkhanza moti mpaka mwina moyo wa munthu umatha kupita.
“Mwana akabadwa ndi ziwalo zodabwitsa akuluakulu ankatha kumupitiriritsa dala m’chikuta momwemo moti nthawi zina mayi wake sankazindikira. Ena ankakhulupirira kuti mwanayo amabweretsa mavuto. Amatha kumupitiriritsa dala n’kukanena kuti wabwera wakufa kale,” akutero Kwitanda.
Koma Dr Adamson Muula, mmodzi mwa adotolo a nthenda zofala, wati si bwino kuchotsa moyo wa mwana pongotengera momwe akuonekera, polingalira kuti moyo ndi chimodzimodzi, osalingalira za momwe khanda likuonekera.
“Funso loti tidzifunse ndi loti kodi kuoneka mosiyana ndi ena kungapangitse khanda kuti lisakhale munthu? Khanda lobadwa mwa mayi ndi bambo ndi munthu basi. Kodi tikapha ana obadwa mosiyana ndi ena, kenako tidzapha ndani?” akudabwa Muula.
Mmodzi mwa akadaulo oona za momwe anthu amaganizira Symon Chiziwa akuti nkhani ya ana obadwa modabwitsa yakhala ikuzunguza anthu ambiri padziko lapansi.
“Ana otere akabadwa kumakhala manong’onong’o. Nthawi zambiri azamba amangowasiya anawo kuti afe. Makolo amangouzidwa kuti anawo apitirira,” akutero Chiziwa.
Iye wati ena amakhulupirira kuti makolo akhoza kuvutika kwambiri kusamalira ana otere, komanso kuti akhoza kuwabweretsera matsoka.
“Kalekale ku Greece ana otere akabadwa amatsamwitsidwa kapena kumizidwa. Mwana akabadwa, makolo amayenera kupititsa anawo kwa akuluakulu ndipo akaona kuti kalibe ndi moyo wamphamvu, amakasiya poyera chifukwa amati sikadzakhala nzika yodalirika,” iye akutero.
Koma izi zili choncho, Chiziwa akuti anthu amadziwa kuti moyo ndi chinthu chamtengo wapatali choncho ‘kukonza’ makanda chifukwa cha ichi n’kulakwa.
“Makolo amakhulupirira kuti akabereka, alera ana kuti adzaime paokha. Ana otere zikhoza kukhala zovuta kuti adzaime paokha. Choncho nkhaniyi ndi yofunika kufunsa makolowo maganizo awo,” akutero Chiziwa.
Malamulo a dziko lino amapereka ufulu wokhala ndi moyo kwa munthu aliyense.
Gawo lachinayi la malamulo oyendetsera dziko lino limati: “Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo ndipo palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zochotsa moyo wa mnzake pokhapokha imfayo yagamulidwa ndi khothi lodziwika bwino litamupeza munthu woti aphedweyo ndi mlandu wofunika kulandira chilango chotero potsatira zomwe malamulowo akunena.”
Mkulu wa Bungwe la anamwino ndi azamba m’dziko muno Harriet Kapyepye wati mchitidwewu unali wozunza mizimu ya anthu osalakwa pogwiritsa ntchito mfundo zopanda pake.
Iye adati aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo ngakhale atabadwa ndi vuto lalikulu chotani.
Kapyepye wati anamwino ndi azamba am’dziko muno amaphunzitsidwa mmene nkhanza zoterezi zingapeweredwe komanso amaphunzitsidwa mmene angalangizire amayi omwe amapempha okha kuti mwana yemwe wabadwa ndi chilema amuphe komanso kuti amulandire m’banjamo.
“Ife pantchito yathu timaonetsetsa kuti mwana aliyense yemwe wabadwa akhale ndi moyo komanso asanyozeke chifukwa cha chilema. Tili ndi mabungwe osiyanasiyana omwe timatha kutumizako ana amavuto ena ndipo amatha kukonza mavuto ngati amenewo,” akutero Kapyepye

1 comentário:

Anónimo disse...

If the handler pasѕes the process, they аre requiгed to complete a 10-week bаsic couгse ωith their
asѕіgned K-9. Here thе pгojeсt іѕ аnаlуzеd negotiating the
turn arоunԁ time. Cаreful therapy сombined
with а combinatіon of theraрies cаn allеѵiatе PSD sуmptoms
anԁ helр motheг stay in shape to hаve a
safe and healthy natural birth. Precіsе slicing helps in revealing the сleаn аnd aρt coding structuгes fοr thе website, whiсh playѕ a
key гole in the peгformаnсe of the website on various popular ωeb browsers
and ѕearсh engines. Word - Press is a lеading сontent management ѕystem
now ωith sеveral design toοls and сustοm themes.
Μayor Miсhael Nuttеr, Pennsуlvania's Secretary of Education Ron Tomalis and the SRC announced on Tuesday, October 4ththat they have created full-time Executive Advisors, Financial Operations and a Systems Working Group that will help with the reform of the Philadelphia School District.

Here is my homepage ... psd kids games